DR MICHAEL USI ALEPHERA KUCHITITSA MTSONKHANO
Mtsogoleri wachipani cha odya zake alibe mulandu (OZAM), walephera kuchititsa mtsonkhano pa PIM trading centre m'boma la chiradzulu, kutsatira kubweranso Kwa yemwe akufuna kuyimira ngati phungu mchipani cha DPP.
Poyankhulapo omwe anayandikira pamalopa omwenso ndi mmodzi mwa ochita malonda pamalopa, miss Catherine chingwalu, anati, " mtsogoleri wachipani cha OZAM a Dr Michael USI, anabwera pamalopa kuti ayankhule ndi anthu a mderali ndipo anayamba kugawa ndithu ma t shirt komanso nsalu zachipanichi."
"Ali mkati mogawa nsalu ndi ma t shirt amenewa kunatulukira galimoto ya yemwe akuyimira ngati phungu mchipani cha DPP zomwe zinachititsa kuti Dr Michael Usi anyamuke pamalopa Poona kuti munthu wina wafika kale zomwenso zikanayambitsa mpungwepungwe pamalopa." Iwo anapitiliza.
Izi sizololedwa mmalamulo a zinsankho, pamene bungwe loyendetsa zinsankho la mec limalimbikitsa mtendere m'misonkhano yokopa anthu.
By Jones busuman.
Comments
Post a Comment